
Wolemba Stella Chasowa
Komishonala wa Bungwe la MEC Emmanuel Fabiano wati ndiokhutira ndi momwe ntchito yotsimikiza mayina mukaundula wa voti yayambira m’boma la Salima
Iye wayankhula izi lachiwiri atayendera malo amene kukuchitika ntchito yotsimikiza mainayi m’bomali
Fabiano anati malo omwe iye wayendera chilichonse chikuyenda bwino ndipo sanalandireko dandaulo lililonse.
“Pakadali pano mmalo omwe ndapitapo palibe pomwe ndauzidwa kuti panali dandaulo kapena vuto lina lilonse kwa anthu omwe akudzatsimikiza maina awo” fabiyano watero
Iye anapitiriza kumema atsogoleri azipani kuti atumize nthumwi zawo pa malo omwe pakichitikira ntchitoyi.
Gawo loyamba lotsimikiza maina mu kaundula wa mavoti layamba lachiwiri pa 13 May ndipo litha pa 15 May 2025.