Bambo amangidwa chifukwa chomenya mkazi wake ndi chitsulo.

Wolemba Alice Lissa Kamwanje.

Apolisi m’boma la Salima amanga bambo wa zaka 24 zakubadwa a Kumbukani Wedi chifukwa chovulaza mkazi wawo zomwe zapangitsa a chipatala kuchotsa diso lake kamba kovulala.

Mneneri wa apolisi m’bomali Sub Inspector Rabecca Ndiwate wati bamboyu anamenya mkazi wake pomukaikira ndikomwe anatenga ndalama yogulira koilo.

A Ndiwate wati bamboyu anamumenya mkaziyu m’maso ndi chitsulo zomwe zinapangitsa kuti avulale kwambiri diso.

Pakadali pano apolisi alimbikitsa anthu omwe akukumana ndi nkhaza kuti azikanena ku polisi Kuti apeze thandizo ndi upangiri pofuna kuchepetsa nkhaza.

A Kumbukani Wedi amachokera m’mudzi wa Ntochera mfumu yaikulu Pemba m’boma la Salima.

Related posts

Salima District joins global GBV commemoration.

‘Adopt the Needy Students’ Initiative Unveiled at UNIMA Alumni AGM.

10 Years imprisonment for breaking a house.