Anthu apemphedwa kutsatira njira zopewera zibayo.

Wolemba Christina Mdolo.

M’modzi mwa madokotala pa chipatala chachikulu cha m’boma la Salima a Mercy Mawazo wapempha anthu okhala m’bomali kuti apewe kukhala m’malo odzaza anthu ambiri pofuna kupewa matenda a chibayo.

A Mawazo ayankhula izi pomwe dziko lino lalowa munyengo yozizira, nthawi yomwe matenda a chibayo amakhala ochuluka.

Iwo ati matenda a chibayo amatha kufalikira kudzera m’malovu amene amatuluka munthu akatsokomola.

Iwo alimbikitsanso anthu a m’boma la Salima kuvala zovala zotentha panthawi ino kuti adziteteze ku nyengo yozizira, kusamalira ukhondo posamba m’manja ndi sopo nthawi zonse, kumwa madzi okwanira pafupifupi malita awiri patsiku, komanso kudya zakudya zopatsa thanzi zochokera m’magulu asanu ndi limodzi a zakudya.

Chibayo ndi matenda amene amakhudza mapapo, pomwe timatumba ta mpweya m’mapapo timadzaza ndi madzi kapena mafinya.

Matendawa amayambitsidwa makamaka ndi mabakiteriya, ma virus kapena mafangasi.

Chibayo chimatha kuyambitsa zizindikiro zosiyanasiyana kuyambira kutsokomola ndi kutentha thupi pang’ono mpaka kuvutika kwambiri kupuma, zomwe nthawi zina zingakhale zoopsa pa moyo wa munthu.

Related posts

Bambo amangidwa chifukwa chomenya mkazi wake ndi chitsulo.

Salima District joins global GBV commemoration.

‘Adopt the Needy Students’ Initiative Unveiled at UNIMA Alumni AGM.