
Wolemba Liana Bonongwe
Bungwe la world vision Malawi lapeleka ufa wa phala wa likuni wandalama zokwana 28 million kwacha ku sukulu ya mkombaphala ya Chigumukire m’mudzi wa mkhukhi M’boma la Salima.
Poyankhula atapeleka thandizoli, Chikumbutso kamwendo yemwe ndi mkulu oyang’anira ma pulogalamu a bungwe la world vision mmaboma a Salima ndi Dedza, Wati bungwe lawo linakhazikitsa ndondomeko yogawa phalali pofuna kukwanilitsa masomphenya awo othetsa njala maka Kwa ana ang’onoang’ono omwe amanyetchera.
Kamwendo wapempha adindo onse kuphatikizapo omwe amasamalira ana mu msukulu za mkombaphala kuti asamazembetse kapena kugulitsa phalali, ndipo opezeka akuchita Izi lamuro lidzagwira ntchito.
Poyankhulapo phalali litapelekedwa, mfumu ya derali a Khukhi, wati ndiothokoza world vision kamba Ka thandizoli ndipo wati awonetsetsa kuti pasapezeke ozembetsa phalali kupititsa mmakomo kapena kugulitsa.

1 comment
Good https://lc.cx/xjXBQT