
Chithunzi Adams Cuba Phiri.
Wolemba Liana Bonongwe
Adams Curba Phiri ndiye wapambana pa udindo wa wapampando wa Salima district football association (SADFA) atagonjetsa yemwe anali wapampando wabungweri Abdul Salaam Mtimbwinda ndi ma vote 33 kwa 9.
Chisankhochi chachitika loweluka ku Matenje Teachers Development Center (TDC) pomwe nthumwi zotsatira masewero a Mpira kuchokera muma zone onse a m’boma anaponya vote.
Sheikh Ibrahim Omar ndi amene apambana pa udindo wa wachiwiri kwa wapampando opanda opikisana naye.
Mu mkuyankhula kwake atapambana Phiri wati agwira ntchito ndi aliyese pofuna kupititsa patsogolo mpira m’boma la Salima.
Iye wati ali ndi masomphenya obweletsa team ya Nyasa Big bullets kuzakumana ndi team yochokera m’boma la Salima pamene Bwalo la zamasewero la Community lizidzatsegulidwa.
