
Chithunzi: Enock Phale
Wolemba Chisomo Mpaso
Phungu wa dera laku mpoto chakumadzulo m’boma la Salima Enock Phale wati ali ndi chikhulupiliro kuti anthu aku dera kwake amuvotelanso chifukwa wakwanilitsa zitukuko zomwe analonjeza chipambanileni pazisankho za chaka Cha 2019.
Poyankhula ndi Wailesi ya Love lachinayi, Phale wati munthawi yake wabweletsa zitukuko zochuluka zomwe zapindulitsa miyoyo ya anthu monga kumanga ma midada ya sukulu zomwe zapititsa maphunziro patsogolo, kumanga zipatala komanso kuzonza misewu zomwe zapangitsa Mayendedwe kukhala osavuta.
Iye anatchula za kumangidwa kwa chipatala cha m’nema kudera la mfumu yaikulu Makanjira ndi thandizo lochokela kundalama za GESD kunathandiza kuchepetsa imfa za amayi omwe amavutika kupeza thandizo lachipatala chifukwa Cha kutalika kwa mtunda.
Iwo anatchulanso kumangidwa kwa ofesi ya aphunzitsi ku Chitala ndinso ofesi yoona za malimidwe ya Matenje EPA mongotchula zochepa.

chithunzi: Joseph Kandiyesa
Woyankhulapo pa nkhani zochitika chitika kuchokera m’boma la Salima a Joseph Kandiyesa anayamikira Phunguyu kamba ka zitukuko zomwe zikuoneka.
Komabe a Kandiyesa apempha anthu ochokera kumpoto chakumadzulo m’boma la Salima kuti adziwe ubwino osasinthasintha mtsogoleri chifukwa izi zimathandiza kupeleka mpata kuti mtsogoleri amalize zitukuko zomwe sizinamalizidwe.
Potengela ntchito yolembanso madera, Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC), a Phale akaimira kudela lawo lomwe tsopano ndi pakati chakumadzulo kwa boma la Salima (Central West).