Ophunzira pa Sukulu ya Chagunda asimba lokoma

Wolemba Stella Chasowa

Pali chiyembekezo chakuti ophunzira pa sukulu ya Chagunda akhala ndi zipinda zophunzirira zabwino pomwe phungu wanyumba yamalamulo wa derali Mike Mwawa wayamba kubweretsa zipangizo zomangira chipinda pa sulukuyi.

Ophunzira pa Sukulu ya Chagunda akhala akugwiritsa ntchito tchalitchi komanso nyumba zoyandikana ndi sukuluyi ngati malo ophunzirirapo kamba ka kuchepa kwa zipinda zophunziriramo.

Mwawa wati ntchito yomanga malo ophunziliramoyi imayenera kuyambika masabata a mbuyo koma zidakanika kamba koti kontilakitala anatanganidwa ndi zina, koma watsimikizira anthu a derali kuti ntchitoyi iyamba sabata ya mawa.

Mwawa anapititiza kunena kuti pomanga zipinda zophunzilirazi aonjezeranso zipinda zina zitatu.

Pakadali pano mphunzitsi wamkulu pa sukulu ya Chagunda, Jason Misoya watsimikiza za kufika kwa zipangizo zomangirazi monga njerwa za simenti.

Sukulu ya pulayimale ya Chagunda ili ndi ophunzira 1264 a sitandade 1 mpaka 8.

Related posts

Health Initiative Restores Sight to Salima Residents.

Sengabay hunger stricken families shot in the arm

Amangidwa atapezeka ndi Chamba.

1 comment

Harper2997 April 27, 2025 - 10:20 am
Very good https://t.ly/tndaA
Add Comment