
Ntchito za umoyo m’boma la Salima ziyembekezeleka kupita patsogolo kamba kathandzo lomwe bungwe la Institute of Marketing in Malawi lapereka pa chipatala chachikulu cha Salima loweluka pa 25 October 2025.
Thandizoli lomwe ndi lakatundu wandalama pafupifupi 10 miliyoni kwacha lapelekedwa ku chipatalachi ngati mbali imodzi yanthambi za chifundo za bungweri pomweso akuchita nkumano wawo waukulu wapachaka.

Poyankhula ndi wayilesi ya Love, pulezidenti wa bungweli George Damson wati ali ndichikhulupiliro kuti katunduyu asamalidwa bwino komaso sipapezeka nchitidwe uliwose wa umbanda ndi katangale.
“Tili ndi chikhulupiliro chakuti katunduyu wafika malo oyenelera komaso asamalidwa bwino” Damson anafotokoza.
Iwo anapitiliza kunenaso kuti ntchito zachifundozi sikuti zathela pompa koma zipitilirabe.
Ndipo mawu ake mkulu woyang’anira madotolo m’boma la Salima, Dr Steve Kumwenda, ayamikira thandizoli ponena kuti liwathandiza munjira zambiri zakagwiridwe tchito kawo pa chipatalachi. Iwo sanabise mawu koma kuthokozaso bungweli ponena kuti thandizoli lafika munthawi yake kamba kakuti zipangizo zina zangowonongeza posachedwa ndipo analibe ntengo ogwira.
Bungwe la Institute of Marketing in Malawi mwazina lapeleka ma bedi ogona odwala, njinga zonyamulira odwala, zipangizo zothandizila kupuma komaso mankhwala otsukira zilonda mwa zina.
Chipatala cha chikulu cha Salima chimathandiza anthu oposela 5000.
Wolemba enjamin Kumphanje.