
Wolemba Chisomo Mpaso
Bungwe lophunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana la National Initiative for Civic Education (NICE) m’boma la Salima ladandaula ndi kusapezeka kwa aphungu omwe akuimira pachisankho ku dera lakummwela kwa bomali pa mtsutso omwe anakonza.
Mkulu wa ofesi ya NICE, Queen Mataya wati aphungu asanu ndi awiri omwe anavomeleza kuti abwera, m’modzi yekha ndiyemwe anapezeka ku mtsutsowu.
Mataya wati ndikhumbo lawo kupereka mwayi kwa aphungu onse komanso makhansala kuti apeleke nfundo zawo komanso kuyankha mafunso kwa anthu.
“Tsiku loyamba mtsutso tinali ku pa ofesi ya aphunzitsi pa Chipoka pomwe makhansala anabwela ochuluka koma mbali ya phungu anabwela mmodzi,” Mataya anatero.
Woyankhulapo pa nkhani zochitika m’dziko muno a Joseph Kandiyesa wapempha opikisana nawo pa mipandoyi kugwilitsa ntchito mwayi omwe bungwe la NICE lapereka.
“Aphungu komanso makhansala ali ndi mwayi oti akhoza kuyankha mafunso omwe anthu amakhala nawo kusiyana ndi pansonkhano pomwe aliyense amangonva zonena zawo,” Kandiyesa anatero.
Mtsutso ukupitilila madela ena mpaka pa 23 August 2025.