
Wolemba William Chitengu
Unduna owona za chilengedwe ndikusintha kwa nyengo kudzera ku nthambi yoona za nkhalango, walengeza kutseka kwa nyengo yodzala mitengo ya mchaka cha 2024/2025 yomwe idatsekulilidwa ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Micheal Usi pa 17 December chaka chatha ndipo yatsilizika pa 15 April chaka chino.
Malingana ndi kalata yomwe wasainira ndi mlembi ku Undunawu, Dr Yusuf M. Mkungula, undunawu ndiokondwa ponena kuti mitengo yopitilira 50 Milllion mdziko muno ndiyomwe yadzalidwa mumalo okwana ma hekitala 9 640.6 .
Undunawu wapempha anthu amene ali kumadera kumene mvula ikugwabe komaso kumene kuli chonde chabwino kuti apitilize kudzala mitengo komanso wapempha ena onse okhudziwa kuti asamalire mitengo yomwe yabzalidwayi.
Nyengo yobzala mitengo ya 2023/24 yasonyeza kuti mitengo yokwana 60% ndi imene yapulumuka ku ng’amba komanso kudyedwa ndi Ziweto.