
Atengambali pa Mkumanowu.
Wolemba William Chitengu Jnr
Bungwe loyendetsa komanso kuyang’anira masewero a mulosera mdziko muno la Malawi Gaming and Lotteries Authority (MAGLA), likuchititsa nkumano ndi ma kampani ochititsa masewerowa m’boma la Salima pazakufunika kotsatira ndondomeko za tsopano zomwe zaikidwa komanso kutsatira njira za makono zoyendetsera masewerowa.
Mkulu wa board ya MAGLA, Fredrick Changanya watsindika kufunika kotsatira ndondomeko pakati pa makampaniwa ndipo ali ndi chiyembekezo kuti nkumanowu uthandizira kuti azitsatira.
“Pali malamulo ena omwe akhazikitsidwa posachedwa okhudza kayendetsedwe kamakono pogwiritsa ntchito zinthu zamakono komanso kaseweredwe ka masewerowa ndipo ndizofunika kwambiri kuti ma kampani azidziwe komanso atsatire moyenera ndipo taitana akatswiri kuchokera mdziko la South Africa omwe ndi achiyamba kale pa nkhani zoyendetsa masewero a muloserawa.” Changanya anafotokoza.
Iye anapitiliza potsindika za kufunika koti makolo akhale patsogolo kuwonetsetsa kuti ana awo osapyora zaka 18 asasewere masewerowa pakuti izi zingasokoneze kaganizidwe kao ndipo wapempha osewera masewerowa kuti azindikire kuti iyi sinjira yopezera ndalama koma ndi masewero chabe.
Mkulu wa kampani ya Mini Monte Gaming Limited, Madalitso Gongwa wati nkumanowu ndi othandiza kwambiri.
“Mkumano utipindulira pankhani ya njira, komanso kayendetsedwe ka makono ka masewerowa kuti tipititseso masewero a mulosera patsogol” a Gongwa anafotokoza.
Ena mwa makampani omwe ali nao pa nkumanowu ndi monga 888 Bets, Bet Pawa, Premier Bet.

1 comment
Awesome https://t.ly/tndaA