
Wolemba Chisomo Mpaso.
Pamene m’dziko muno mukhale mukuchitika chisankho cha patatu mawa pa 16 September, Kampani yogulitsa magetsi ya Escom yati iwonetsetsa kuti magetsi asazimezime m’masiku anayi ndi cholinga choti anthu adzalandire zotsatira za chisankho popanda zovuta zilizonse.
Mkulu wa Kampani ya Escom Kamkwamba Kumwenda wayankhula izi lolemba pa 15 September pa nsonkhano wa Atolankhani mu mzinda wa Blantyre.
A Kamkwamba ati apempha ma kampani ena akulu akulu omwe amagwilitsa ntchito magetsi kuti azimitse Kaye makina awo monga tsiku la tchuthi kuti achulukitse mphamvu ya magetsi omwe adzafunike pa tsikuli.
“Pali ma kampani ena omwe tawapepha ndipo avomela komabe ena sanavomele koma tipitiliza kukamba nawo popeza tsikuli ndilofunika kwambili ku dziko lino,” Iwo anatero.
Poyankhulapo pa nkhaniyi mkulu wa kampani yopanga magetsi ya egenco Engineer Maxon Chitawo ati awonetsetsa kuti makina onse opanga magetsi akugwila ntchito munthawiyi.
Kampani Ya Escom ikuyembekezera kuthana ndi mavuto akuzimazima kwa magetsi ndi thandizo la ndalama zokwana 250 Million USD zochokera ku World Bank kuti zifikile anthu okwana 250,000 mu zaka 5 zikubwelazi.