
Wolemba Chisomo Mpaso
Katswiri pa nkhani zamalimidwe Leonard Chimwaza wapempha alimi m’dziko muno kuti aonetsetse kuti mitengo yogulira mbewu yomwe yangotulutsidwa kumene ndi boma ikutsatidwa.
A Chimwaza ati ndikofunikira kuti alimi asamagulitse mbewu zawo kwa anthu omwe ndiosavomelezeka maka mavenda omwe amagulitsa mbewuzi kunja kwa dziko lino.
Iwo ati mchitidwewu ndi omwe ukukolezera njala m’dziko muno kwa zaka zochuluka.
Kalata yomwe yasainidwa ndi mlembi wa mkulu mu unduna wazamalimidwe Geoffrey Mamba yachenjeza mavenda omwe amagula mbewu kwa alimi motsika ponena kuti athana nawo.
A Mamba alangizanso anthu omwe akufuna kugula mbewu kwa alimi kuti atenge ziphanso zowaloleza kugula mbewu muma office a zigawo monga Kasungu, Salima, Lilongwe, Karonga ndi Blantyre kungotchulapo ochepa.
Chimanga chaikidwa pa Mtengo wa 1050, mpunga osapuntha 1200 kwacha, nyemba zosasakaniza 2500, mtedza uli pa 2500 pa kilogilamu imodzi kungotchulapo zochepa.
Chaka chatha Chimanga chinaikidwa pa mtengo wa 650 kwacha pa kilogilamu imodzi.
