
Alimi omwe amachita Ulimi wa mthilira ochokera m’mudzi mwa Group Village Mtende Mfumu yaikulu Pemba m’boma la Salima apempha boma kuti liwathandize kupeza misika yovomelezeka yogulitsira zokolola zawo.
M’modzi mwa alimi a Lithipe Club Edrina Kenamu wati zokolola zawo amagulitsa kwa ma venda omwe amagula pa mitengo yosavomelezeka ndi boma ndipo ma vendawo amapeza phindu lochuluka.A Kenamu ayankhula izi lachinayi pomwe bungwe la World Relief linakonza zionetsero za malonda m’derali.

Mkulu owona ntchito za Ulimi m’boma la Salima Reuben Banda walangiza alimiwa kupezelatu misika ya zomwe akulima kuti asamasowe misika.
Iwo anati alimi akadziwilatu yemwe adzagule mbewu zawo zimathandiza kuti ogula asanyinyilike kumbali ya mitengo.Poyankhulapo yemwe amayang’anira ntchito ya ma pulogalamu komanso kapezedwe ka chuma ku bungwe la World Relief Thokozani Banda wati ndiokondwa ndizotsatira za zionetselozi pomwe alimi akumana ndi atenga mbali osiyana siyana omwe agula komanso kugulitsa malonda awo.
Iwo anati ngati mbali imodzi yofuna kuthandiza anthu okhala m’derali maka ku mbali ya ngozi zogwa mwa dzidzidzi zomwe zimakhudza mbewu, anaganiza zothandiza Ulimi wathilira.
Bungwe la World Relief likugwira ntchito kwa mfumu yaikulu Pemba komanso Ndindi mu pulojekiti ya Climate just community ndithandizo la Scottish government komanso Oxfam yomwe ndiya zaka zitatu.