
Lumbani Mgula
Wolemba Chisomo Mpaso.
Pamene zisankho zapatatu zikuyandikila mmwezi wa September pa 16, Bungwe la Umunthu Plus laphunzitsa gulu la amayi ochokela mmadela osiyana siyana m’boma la Nkhotakota za momwe angathanilane ndi mikangano yomwe imadza pakati pa anthu.
Lumbani Mgula yemwe ndi mkulu wa ofesi yoyang’anira ndi kuunikira ntchito za bungwe la Umunthu Plus wati Iwo amakonza maphunziro ophunzitsa amayi chifukwa ndi amene amakhudzidwa kwambiri ndi mikangano yomwe imadza mbali zonse.
A Mgula anaonjezera kuti amayi ambiri amapezeka muzochitika zosiyana siyana m’dziko kotero upangiri wa momwe angathanilane ndi mikangano ukafika kwa anthu ochuluka.
M’modzi mwa atenga mbali omwe amapeleka maphunzilo kwa amayiwa, Oweluza Milandu Dumisani Kadobelere Katundu kuchokela ku bwalo loweluza Milandu m’boma la Nkhotakota anati kuphunzitsa amayi ochokela m’madera za momwe angathetsere mikangano kuchepetsa chiwelengero Cha Milandu yomwe imabwera ku mabwalo amilandu.
A Katundu anati milandu yambiri ikhonza kuweluzidwa ku madera komwe anthu amakhala, komanso kuchepetsa nthawi yomwe milandu imatenga kuti iweluzidwe.
M’modzi mwa amayi omwe anali nawo pa mkumanowu, omwe ndi achiwili kwa Khala pa mpando wa zokambilana za amayi kuchokera kwa Malenga chanzi Ester Pansanje wathokoza bungwe la Umunthu Plus powapatsa maphunziro, ndipo wati awonetsetsa kuti akuwagwilitsa ntchito popeza Iwo anakhudzidwa ndi mikangano yochuluka ku madera.

M’modzi mwa atengambali