
Wolemba William Chitengu Jnr
A Polisi m’boma la Salima amanga abambo atatu kamba kopezeka ndi chamba opanda chilorezo.
Malingana ndi Mneneri wa polisi ya Salima, Sub inspector Rabecca ndiwate abambo atatuwa agwidwa usiku wapa 25/26 April 2025 pamene apolisi anaika malo ochitira chipikisheni pafupi ndi malo omwetsera mafuta a mlamba mseu wa Salima-Balaka.
Oganiziridwa oyamba a Mickson Thomson azaka 37, awanga potsatira a polisi kufufuza galimoto yomwe amayendera ndipo anapeza thumba lomwe munali chambachi.
A Mathews Mafuta a zaka 40, komanso a Happy Chiumia a zaka 27, amangidwa pamene amafuna kuzembetsa chambachi pogwiritsa ntchito njinga za moto.
Atatuwa akaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa pamene akayankhe milandu yokhudza nkhaniyi.
2 comments
Very good https://t.ly/tndaA
Very good https://t.ly/tndaA