
Chithunzi: James Manyetera
A James Manyetera omwe amafuna kupikisana nawo pa zisankho za Chipulula za Chipani cha Malawi Congress (MCP) ati asintha ganizo lawo ndipo adzaima ngati phungu oima payekha dera lapakati m’boma la Salima.
Poyankhula mwapadera ndi wailesi ya Love, a Manyetera ati kuchedwa kupeleka maina a anthu omwe akuyenera kuvota ndikumene kwapangitsa kuti iwo asinthe ganizo lawo.
Iwo ati ndondomeko ya zisankho yomwe yaikidwa ikukomera phungu yemwe akadali pano popeza apatsidwa maina a anthu oponya kutakhala tsiku limodzi.
“Ndine okhumudwa ndi ndondomeko zomwe Chipani chinaika, munthu amene ndikupikisana naye ndi amene ali ndi ma madera omwe akudzavota. Kufika lolemba la Sabata ino yomwe maderawa anapelekedwa ku kwa adindo a pa Boma. Madandaulo onse ku Chipani sanaveke kuti tikhale ndi nthawi yokumana ndi ma madera oponya voti”, a Manyetera anatero.
Iwo ati ngakhale aima paokha koma akanalibe membala wa Chipani Cha Malawi Congress ndipo atsimikiza kuti sakusunthika.
Tinayesa kufuna kuyankhula ndi mkulu owona za Chisankho mu Chipani cha Malawi Congress, Dr. Elias Chakwera komanso mneneri Dr Jessie Kabwira koma lamya zawo za manja sizimayankhidwa.
Zisankho za Chipulura za Chipanichi zichitika mawa pa 19 April ndipo malingana ndi a Manyetera adziwa za izi nthawi itatha kale.

1 comment
Awesome https://t.ly/tndaA