Mafumu Achenjezedwa pa mitengo ya Mbewu.

Senior Group Sosola

Bungwe la Malawi Chewa Heritage (MACHE) lachenjeza mafumu kuti asachite mchitidwe wolanda ndalama kwa anthu ogula mbewu pofuna kuti alimi azigulidwa mbewu zawo pa mtengo wotsika.

Wapampando wa Bungweli Senior Group Sosola wati mafumu ali ndi udindo woyang’anitsitsa kuti ogula mbewu akugula pa mtengo woyenera ndikupeza phindu pa zokolola zawo.

Asosola ati ndizodandaulitsa kuti mafumu ena amaonelera alimi akugulidwa mbewu pa mitengo yosavomelezeka komanso pa sikelo zomwe ndizosavomelezeka ndi bungwe la Malawi Bureau of Standards.

“Pali mafumu ena a Chichewa amene amalolera kulandira ndalama Kwa ogula polera kuti alimi azigulidwa pa mtengo otsika, enanso amalola ogula kugulitsa ntchito sikelo zosavomelezeka ndi bungwe loona za miyezo la MBS”, anatero a Sosola.

Iwo ati mafumu atenge gawo poonetsetsa kuti alimi akudyelera thukuta limene akhetsa pogulidwa mbewu pa mtengo wabwino.

A Sosola atsindikanso kufunika Kwa m’gwirizano pakati pa a Chewa m’dziko muno ponena kuti muumodzi muli mphamvu.

Bungwe la Malawi Chewa Heritage linakhazikitsidwa mu Chaka cha 2023 pofuna kuthana ndi mavuto omwe a Chewa amakumana nawo.

Related posts

Ntchito za Umoyo zipita patsogolo pa chipatala cha Salima.

Deputy minister of Health launches FHS

Mitengo yoposa 50 million yabzalidwa

2 comments

Diana2572 April 26, 2025 - 12:30 am
Gabriella4731 April 27, 2025 - 1:41 am
Add Comment