Wolemba Liana Bonongwe
Ofesi yowona za chisamaliro cha anthu m’boma la Salima yati ndi yokhutira ndi momwe ntchito yopelekera ndalama za mtukula pakhomo kudzera pa lamya ikuyendera komaso momwe anthu akupundulira ndi ndondomekoyi m’bomali.
Woyendetsa ntchito za chisamaliro cha anthu komanso kuona ntchito za mtukula pa khomo ku khonsolo ya Salima, Thumbiko Mbale wati anaganiza zokayendera anthu omwe akupindula ndi mtukula pakhomo, ndicholinga choti akamve momwe akupindulira ndi ndalamazi komaso mavuto omwe akukumana nawo.
Iye anati anthu ambiri apindula ndi ndondomekoyi, monga kugula chakudya, ziweto za pakhomo komaso kukwanitsa kulipirira ana Ku sukulu.
Omwe amapindula ndi ndondomekoyi Felesta Yohane ochokera mmudzi wa Ngolowindo komaso Adawa Mwamadi ochokera mmudzi wa Kundayi anati Iwo ndi othokoza Boma ndi ndalama zomwe amalandirazi komaso ndalama ina yomwe anawaonjezera yokwana 70,000 kwacha yomwe amagulira chimanga.
Amayiwa apempha woyendetsa ntchito za mtukula pakhomozi, kuti akafikireso ena ndi thandizoli. Komaso kumema azawo kuti azingwiratsa ntchito bwino ndalamazi kuti azipindula nazo.