Wolemba Chisomo Mpaso.
Anthu okhala mmudzi mwa Kawangila mfumu yaikulu Khombedza m’boma la Salima komanso midzi ina yozungulira apempha Bungwe la Amref Health Africa kudzera ku Unduna wa zaumoyo kuti awathandize ndi chipatala pafupi.
Poyankhula lolemba pambali pa ntchito yopeleka thandizo la chipatala choyendayenda, m’modzi mwa anthuwa a Violet Damiton ati izi zithandizira kuti azipeza thandizo la chipatala mosavuta.
A Damiton ati anthu ambiri amayenera kuyenda mtunda wa ma kilomita 27 kuti akafike ku chipatala cha Makiyoni zomwe zimakhala zovuta chifukwa cha mayendedwe abwino.
Thandizo la chipatala choyendayenda limabwera m’mudzimu kamodzi pa mwezi mothandizidwa ndi ndi bungweli.
M’mawu ake mkulu woyang’anila, bungwe la Amref ku Africa, Hester Kwinda Nyasulu ati amapeleka thandizo la chipatala kwa anthuwa pozindikira za ufulu wawo okhala ndi moyo wathanzi.
A Nyasulu ati maso mphenya a boma ndioti anthu azikhala ndi chipatala cha ching’ono pa ma kilomita asanu ndi awiri aliwonse ndipo achita chotheka kukwanilitsa izi.
Mkulu owona zofalitsa nkhani pa chipatala cha Salima, Angella Nyongani Sakwata wayamikira bungweli kamba kothandiza kufikira anthu m’madera okwana asanu ndi pulojekiti yawo.
Iye ati anthu okwana 3,385 ndiomwe amalandila thandizo lachipatala mdela la Kawangila lokha zomwe zikusonyeza kuti anthu ambiri akufunika thandizo la chipatala la pafupi mwamsanga.
Bungwe la Amref liri mu gawo lotsiliza la pulojekiti yawo ya chaka chimodzi yomwe ikupeleka thandizo la chipatala mwazina kulera, sikelo ya ana komanso kupereka thandizo la matenda amgonagona ndi thandizo lochokela ku Pfizer Foundation.