ADINDO ADANDAULA NDIKUCHEDWA KUKONZA MTAYA.

Wolemba: Chisomo Mpaso

Wapampando wa komiti yomwe limayang’anila nyumba yophera nyama pa msika waukulu m’boma la Salima, Ofmed Kapichira wadandaula kamba ka kuchedwa kukonza dzenje lomwe amatayamo nyama yomwe yapezeka kuti ndiyosavomelezeka komanso Tanki yomwe mumalowa madzi oyipa.

Poyankhula ndi Wailesi ya Love, a Kapichilra anati izi zikupangitsa kuti malo ophela nyama wa akhale opanda ukhondo chifukwa madzi oyipawa amatayikila paliponse ndipo malowa saoneka bwino.

Iwo anati akhala akupeleka madandaulo awo ku khonsolo ya Salima yomwe imayang’anila malowa koma sakubwela kudzakonza mwa nsanga.

Mkulu wa ofesi yoona zomangamanga pa khonsolo ya Salima a Harris Kumwenda avomeleza za vutoli ndipo ati khonsolo ili ndi malingaliro omanga dzenje lina komanso kupopa tanki yamadzi yomwe inadzadza, nyengo ya nvula ikafika kumapeto.

A Kumwenda ati mavutowa adza chifukwa chakukwera kwa mlingo wa madzi omwe wadza kamba ka mvula komanso kubadwa kwa “man cover ” zomwe zapangitsa kuti madzi amvula azilowa mosavuta.

Iwo apemphanso anthu okhala madela ozungulira kuti azisamala zipangizo za pamalopa kuti pazikhala posamalika.

Boma la Salima lili ndi malo ophera nyama anayi omwe ndi pa msika waukulu, msika wa Kamuzu Road, msika wa Kaphatenga komanso msika wa Sengabay.

Related posts

Salima District joins global GBV commemoration.

‘Adopt the Needy Students’ Initiative Unveiled at UNIMA Alumni AGM.

10 Years imprisonment for breaking a house.